Asilamu amakhulupilira za tsiku lachiweruzo (tsiku lachimaliziro) pamene anthu onse adzaukitsidwa ku chiweruzo cha Mulungu molingana ndi zikhulupiriro ndi ntchito zawo.

Tsiku lina dziko lapansi lidzatha, ndipo Mulungu adzaukitsa anthu onse akufa kuyambira pachiyambi mpaka kumapeto, ndipo adzaweruza aliyense wa ife payekhapayekha chiweruzo cholungama, molingana ndi Chisilamu anthu opulumutsidwa okha ndi amene anali ndi chikhulupiriro mwa Mulungu woona mmodzi yekha (Ndipo musam’phatikize ndi Mulungu chilichonse pompembedza), ndipo anagonjera ku chifuniro chake, mwa kuchita malamulo ake ndi ziphunzitso zake zimene kwenikweni ziri makhalidwe abwino.