| Mneneri womaliza kudza pambuyo pa Yesu adali Mtumiki Muhammad (SAW).
Iye ndi Mneneri womaliza pa mndandanda wautali wa Aneneri amene adatumizidwa kuti adzaitane anthu kuti amvere ndi kupembedza Mulungu yekha (‘Allah’ m’Chiarabu). |
---|
Yesu ndi Muhammad (SAW) ndi akapolo ndi aneneri a Mulungu amene amatsogolera anthu kuti apembedze Allah. |
Ndi nkhani ya nthawi |
Ndipo Muhammad watumizidwa kwa anthu onse chifukwa iye ndi Mtumiki womaliza wa Mulungu. |
Ngati muvomereza kuti Muhammadi ndi Mtumiki womaliza ndi kutsatira chiphunzitso chake, khulupirirani Yesu, Musa ndi aneneri onse. |
👉Sitimpembedza Muhammadi sitimpembedza Yesu, |
Timangopembedza Mulungu Wamphamvuyonse amene adawalenga . |