#الإيمان_بالكتب
Asilamu amakhulupirira kuti Mulungu adavumbulutsa mabuku kwa atumiki ake monga umboni kwa anthu ndi chiongoko kwa iwo. Mwa mabuku amenewa muli Qur’an yomwe Mulungu adavumbulutsa kwa Mtumiki Muhammad (SAW). Mulungu waikira chitetezo cha Qur’an ku chinyengo chilichonse kapena kusokonekera.